04/09/2026
I was reading some important business ideas on the Facebook ukkhudza za ma youth then I meet with this post by young MP called Tony Anjiba Fletcher akuti adatenga achinyamata from his constituency kupita nawo ku Tanzania kuti akaone mene katundu amakhalira and he write πππππ
Ndinapita kukatenga ambulance nde ndinatenga achinyamata 4 ku constituency kuti akaphunzire mmene anzathu amapangila business ku Tanzania. Awona kuti ku Tanzania kulibe Ulesi, Ndipo anali odabwa kuti Sanawone munthu atalezera mowa mmamawa, kapena masana, anthu onse anali busy kuthamangitsa ma files.
Anthu akulimbira kunjaku, kuthandiza Boma kuti zinthu ziziyenda mudziko.
Aziwa mitengo ya zinthu ngati izi,
1. Ma spare parts a njinga, aziwa kuti ali pa bwanji.
2. Awona mitengo ya zovala mitundu yonse ndi snapato or ma silipasi.
3. Aziwa mmene mateyara a galimoto amatchipila ndi mateyala anjinga za moto:
4. Awonanso katundu wambiri mmene amatchipila.
5. Aziwanso mitengo ya zinthu zamagetsi monda ma sockets ndi zina zotero mmene zimatchipila.
Katundu yense omwe amagulutsidwa kuno amuwona Ndipo awona kuti, kukatenga katundu ku Tz wina aliyense kuzagulitsa kuno ku Malawi ndi business yosadula.
Ndi MK 750,000.00 Ndekuti ndipogona ndi mayendedwe a Munthu mmodzi,
Kenako kukhala ndi ka 1 million kowodera Ndekuti zatheka pamenepo. Kukhala ndi 3million Ndekuti Iweyo uli bwino kwambiri.
Anthu 4 atalandira za give zija, ndikumupatsa munthu mmodzi kuti azawode ngati kuti onse ayika ma shares Ndekuti anthu amenewa akhala ndi shop yogulisa zovala kapena nsapato or ma jersey ampira or ma spares a njinga zamoto mu Cz.
Nkhani ndi yakuti, kukawoda ku Tanzania si business yodula, ndi business yabwino kwambiri Ndipo munthu utha kuchita bwino mwachangu.
NB:Pano sitipanga za ndale koma kutenga zofunikirazo bas I like zomwe walemba komaso ma business ideas
Big up to Hourable π